1 Corinthians 14:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi ngati zipangizo zopanda moyo zimene zili ndi liwu, monga toliro kapena zeze. Woziliza akapanda kusiyanitsa bwino maliwu ake, womvera sangadziŵe nyimbo imene ikuimbidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati chitoliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, chidzazindikirika bwanji chimene chiombedwa kapena kuimbidwa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale mu zinthu zopanda moyo monga chitoliro kapena gitala, zimene zimatulutsa liwu; kodi munthu akhoza kudziwa bwanji nyimbo imene ikuyimbidwa ngati mawu sakumveka mogwirizana bwino?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati toliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, cidzazindikirikabwanji cimene ciombedwa kapena kuyimbidwa?