1 Corinthians 15:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malembotu akuti, “Mulungu adamgonjetsera zinthu zonse.” Koma nchodziŵikiratu kuti pamene akuti “zinthu zonse,” sakuphatikizapo ndi Mulungu yemwe, amene adagonjetsera Khristu zinthu zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Koma pamene anena kuti zonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Mulungu “wayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.” Ponena kuti wayika “zinthu zonse pansi pa mapazi ake,” nʼchodziwikiratu kuti sakuphatikizapo ndi Mulungu yemwe, amene anayika zinthu zonse pansi pa Khristu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ace. Koma pamene anena kutizonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye.