1 Corinthians 15:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati Yesu sadauke kwa akufa, nanga amafunanji anthu amene amabatizidwa m'malo mwa amene adafa? Ngati akufa sauka konse, nanga chifukwa chiyani anthu amabatizidwa m'malo mwao?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati si kutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha iwo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ngati kulibe kuuka kwa akufa, kodi iwo amene akubatizidwa chifukwa cha akufa, adzatani? Ngati akufa saukitsidwa nʼkomwe, bwanji nanga anthu akubatizidwa mʼmalo mwawo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati si kutero, adzacita ciani iwo amene abatizidwa cifukwa ca akufa? Ngatiakufa saukitsidwa konse, abatizidwa cifukwa ninji cifukwa ca iwo?