1 Corinthians 15:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu mau aakulu amene ndidakupatsani ndi omwewo amene inenso ndidalandira. Mauwo ndi akuti Khristu adafera machimo athu, monga Malembo anenera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kuti Khristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti chimene ndinalandira ndinapereka kwa inu monga chofunika kuposa zonse, kuti Khristu anafera zoyipa zathu monga mwa Malemba,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, cimenenso ndinalandira, kuti Kristuanafera zoipa zathu, mongamwa malembo;