1 Corinthians 15:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga pamene ndidalimbana ndi zilombo ku Efeso, ndidapindulapo chiyani, ngati ndinkatsata maganizo a anthu chabe? Ndiyetu ngati akufa sauka, tizingochita monga amanenera kuti, “Tiyeni tizidya ndi kumwa, pakuti maŵa tikufa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati ndinalimbana ndi zilombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, tidye timwe pakuti mawa timwalira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati ndinalimbana ndi zirombo za kuthengo ku Efeso pa zifukwa za umunthu chabe, ndapindulanji? Ngati akufa sadzaukitsidwa, “Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
3 Ngati odinalimbana ndi zirombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, 4 tidye timwepakuti mawa timwalira.