1 Corinthians 15:50 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale, chimene ndikunena nchakuti munthu ndi thupi lake lamnofuli sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu, ndipo zimene zimaola, sizingathe kuloŵa kumene zinthu siziwola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichilowa chisavundi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikunenetsa, abale, kuti thupi ndi magazi sizingathe kulowa mu ufumu wa Mulungu, ndipo zimene zimavunda sizingathe kulowa kumene zinthu sizivunda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinena ici, abale, kuti 16 thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena cibvundi sicilowa cisabvundi.