1 Corinthians 16:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena za mbale wathu, Apolo, ndamuumiriza kolimba kuti pamodzi ndi abale ena abwere kwanuko kudzakuwonani, koma iye sadafune kupita tsopano. Akadzapeza mpata wabwino, adzabwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichinali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene aona nthawi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono kunena za mʼbale wathu, Apolo, ndinamuwumiriza kwambiri kuti abwere kwa inu abale, ndipo iye sanafune kupita tsopano. Koma akadzapeza mpata wabwino adzabwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sicinali cifuniro cace kuti adze tsopano, koma adzafika pameneaona nthawi.