1 Corinthians 16:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale, mukudziŵa kuti Stefanasi ndi a m'banja mwake ndiwo adayambirira kuloŵa chikhristu m'dziko la Akaiya. Ndipo akhala akudzipereka kutumikira anthu a Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choundukula cha Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukudziwa kuti a mʼbanja la Stefano ndiye anali oyamba kutembenuka mtima ku Akaya, ndipo akhala akudzipereka kutumikira oyera mtima. Choncho ndikukudandaulirani, inu abale,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefana, kuti ali cipatsocoundukula ca Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),