1 Corinthians 3:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ntchito za munthu aliyense zidzaonekera poyera, pamene tsiku la chiweruzo lidzaziwonetsa. Pakuti tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito za munthu aliyense.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ntchito yake idzaonekera pamene Tsiku la chiweruzo lidzazionetsa poyera. Tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito ya munthu aliyense.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, cifukwa kuti yabvumbuluka m'moto; ndipo mota wokha udzayesera nchito ya yense ikhala yotani.