1 Corinthians 3:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wina aliyense awononga Nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo; popeza Nyumba ya Mulungu ndi yopatulika ndipo Nyumbayo ndi inu amene.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati wina aononga kacisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti kacisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.