1 Corinthians 3:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zoonadi nzeru za anthu odalira zapansipano, nzopusa pamaso pa Mulungu. Pajatu Malembo akuti, “Mulungu amakola anthu anzeru m'kuchenjera kwao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti nzeru ya dziko lapansi ndi yopusa pamaso pa Mulungu. Monga kwalembedwera kuti, “Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo,”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti nzeru ya dziko ina lapansi iri yopusa kwa Mulungu, Pakuti, kwalembedwa, iye agwira mzeru m'cenjerero lao;