1 Corinthians 4:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga adakusiyanitsa ndi anthu ena ndani? Kaya uli ndi chiyaninso chimene sudachite kuchilandira? Tsono ngati udachita kuzilandira, ukunyadiranji ngati kuti sudangozilandira chabe?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandira?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ndani amakusiyanitsani ndi wina aliyense? Nʼchiyani muli nacho chimene simunalandire? Ndipo ngati munalandira, bwanji mumadzitukumula ngati kuti simunalandire?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli naco ciani cosati wacilandira? Koma ngati wacilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunacilandira?