1 Corinthians 4:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kuti muli nazo kale zonse zimene mumasoŵa! Ndiye kuti mwalemera kale! Ndiye kuti mwasanduka mafumu popanda ife! Ndikadakondwera mukadakhaladi mafumu, kuti ifenso tikhale mafumu pamodzi nanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwadzala kale, mwalemerera kale, mwachita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi muchitadi ufumu, kuti ifenso tikachite ufumu pamodzi ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu muli nazo kale zonse zimene mufuna! Inu mwalemera kale! Inu mwayamba kale kulamulira ife! Ndilakalaka mukanakhaladi mafumu kuti ife tikhale nawo mafumu pamodzi ndi inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M wadzala kale, mwalemerera kale, mwacita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi mucitadi ufumu, kuti ifenso tikacite ufumu pamodzi ndi inu.