1 Corinthians 4:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikuwona kuti atumwife Mulungu adatipatsa malo a kuthungo kwenikweni, ngati anthu oti akukaphedwa. Ndithu tasanduka ngati chinthu chochiwonetsa kwa zolengedwa zonse, osati anthu okha ai, komanso ndi angelo omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti kwa ine zikuoneka ngati kuti Mulungu watiyika ife atumwi pachionetsero, kumapeto kwa mndandanda, monga anthu oweruzidwa kuti akaphedwe mʼmabwalo. Ife tayikidwa kuti tionekere ku dziko lonse, kwa angelo ndi anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife coonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.