1 Corinthians 5:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbiri yawanda ponseponse yonena kuti pakati panu pali dama. Ndipo damalo ndi la mtundu wakuti ndi anthu akunja omwe sachita. Ndamva ndithu kuti munthu wina akukhala ndi mkazi wa bambo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati pa inu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbiri yamveka kuti pakati panu pakuchitika chigololo. Ndipo chigololo cha mtunduwu ngakhale pakati pa akunja sichingapezeke; munthu akumagonana ndi mkazi wa abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwamveka ndithu kuti kuli cigololo pakati pa inu, ndipo cigololo cotere conga sicimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wace.