1 Corinthians 5:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sindiye kuti muziŵapewa anthu onse apansipano amene ali adama, aumbombo, achifwamba, kapena opembedza mafano ai. Kuti mutero kukadafunika kuti mungochokamo m'dziko lino lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
si konsekonse ndi achigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukatuluke m'dziko lapansi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepatu sindikutanthauzatu anthu a dziko lapansi lino amene ndi achigololo, kapena aumbombo, kapena opeza ndalama mwachinyengo, kapena opembedza mafano. Kukanatero mukanangochoka mʼdziko lapansi lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
si konse konse ndi acigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukaturuke m'dziko lapansi;