1 Corinthians 5:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena za ine, ngakhale sindili nanu pamodzi, komabe mtima wanga uli nanu ndithu. Mwakuti ndamuweruza kale munthu amene adachita zimeneziyo, monga ngati ndili nanu pamodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti inedi, thupi langa kulibe, koma mzimu wanga ulipo, ndaweruza kale, monga ngati ndilipo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale sindili nanu mʼthupi, ndili nanu mu mzimu. Ndipo ineyo ndapereka kale chiweruzo pa munthu amene amachita zotere, ngati kuti ndili komweko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti inedi, thupi langa kulibe, koma mzimu wanga ulipo, ndaweruza kale, monga ngati ndiripo,