1 Corinthians 5:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muchotse chofufumitsira chakalechi cha uchimo, kuti mukhale oyera mtima ndithu, ngati buledi watsopano wosafufumitsa, monga momwe muliri ndithu, pakuti Khristu, Mwanawankhosa wathu wa Paska, adaphedwa kale ngati nsembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paska wathu waphedwa, ndiye Khristu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chotsani yisiti wakale kuti mukhale ndi mphumphu yopanda yisiti, monga inu muli. Pakuti Khristu, Mwana Wankhosa wa Paska wathu, anaperekedwa nsembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsukani cotupitsa cakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paskha wathu waphedwa, ndiye Kristu;