1 Corinthians 6:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zinthu zonse nzololedwa kwa ine, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwadi kwa ine, koma sindingalole kuti chilichonse chindigonjetse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mumati, “Ine ndili ndi ufulu wochita chilichonse.” Komatu si zonse zimene nʼzothandiza. “Ndili ndi ufulu wochita chilichonse.” Koma sindidzagonjetsedwa ndi chilichonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula, Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa naco cimodzi.