1 Corinthians 6:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chokha chakuti mumaimbana milandu inu nokhanokha, chatsimikiza kale kuti mwalephereratu. Bwanji osangopirira pamene ena akulakwirani? Bwanji osangolola kuti inuyo akubereni?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamenepo pali chosowa konsekonse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mnzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chokha choti mwakasumirana chikuonetseratu kuti mwagonjetsedwa kale. Bwanji osangolola kuti ena akulakwireni? Bwanji osangolola kuti ena akubereni?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamenepo pali cosowa konse konse mwa inu, kuti muli nayo mirandu wina ndi mnzace. Cifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? simusankhula cifukwa ninji kulolakunyengedwa?