1 Corinthians 6:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kani simudziŵa kuti anthu osalungama sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu? Musadzinyenge: anthu adama, opembedza mafano, achigololo, ochimwa ndi amuna anzao,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi simukudziwa kuti munthu woyipa sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe: achigololo, kapena opembedza mafano, kapena achiwerewere, kapena amuna adama, kapena ogonana ndi amuna okhaokha;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapenasimudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasoceretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena acigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,