1 Corinthians 7:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwa ena mau anga, osati a Ambuye ai, ndi aŵa: Ngati mkhristu ali ndi mkazi wachikunja, ndipo mkaziyo avomera kukhala naye, mwamunayo asathetse ukwatiwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa ena onse ndikunena izi (ineyo osati Ambuye); ngati mʼbale wina ali ndi mkazi wosakhulupirira ndipo mkaziyo walola kukhala pa banja ndi mʼbaleyo, ameneyo asamuleke.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkaziwosakhulupira, ndipo iye abvomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.