1 Corinthians 7:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti mwamuna wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mkazi wakeyo. Nayenso mkazi wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mwamuna wakeyo. Pakadapanda apo, bwenzi ana anu atakhala akunja, koma monga zilirimu, ndi ana a Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo amayeretsedwa chifukwa cha mkazi wakeyo, ndipo mkazi wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha mwamuna wokhulupirirayo. Kupanda apo ana anu akanakhala odetsedwa, koma mmene zililimu ndi oyeretsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mwamuna wosakhulupirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.