1 Corinthians 7:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi iwe, mkazi wachikhristu, ungadziŵe bwanji ngati udzampulumutsa mwamuna wako? Kapenanso iwe, mwamuna wachikhristu, ungadziŵe bwanji ngati udzapulumutsa mkazi wako?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? Kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi iwe, mkazi, ungadziwe bwanji kuti mwina nʼkupulumutsa mwamuna wako? Kapena iwe, mwamuna, ungadziwe bwanji kuti mwina nʼkupulumutsa mkazi wako?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi?