1 Corinthians 7:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense atsate moyo umene Ambuye adamkonzera, moyo umene Mulungu adamuitanira. Ndizo zimene ndimaŵalamula anthu onse amumpingo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika m'Mipingo yonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma aliyense akhale moyo umene Ambuye anamupatsa, umene Mulungu anamuyitanira. Ili ndiye lamulo limene ndalikhazikitsa mʼmipingo yonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika m'Mipingo yonse.