1 Corinthians 7:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m'thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mwamuna wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo chifukwa ichi amatanganidwa kwambiri. Mkazi wosakwatiwa kapena namwali, amalabadira za Ambuye. Cholinga chake ndi kudzipereka kwa Ambuye mʼthupi ndi mu uzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amalabadira za dziko lapansi lino, mmene angakondweretsere mwamuna wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso iye wosakwatiwa alabadira za. Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.