1 Corinthians 7:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikunenatu zimenezi kufuna kuti ndikuthandizeni, osati kuti ndikuletseni ufulu wanu ai. Makamaka ndifuna kuti muzichita zonse moyenera, ndipo kuti muzidzipereka kwathunthu potumikira Ambuye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikunena izi kufuna kuthandiza inu nomwe osati kukupanikizani. Ine ndikufuna mukhale moyenera mosadzigawa pa kudzipereka kwanu kwa Ambuye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ici ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakuchereni msampha, koma kukuthandizani kucita cimene ciyenera, ndi kutsata citsatire Ambuye, opanda coceukitsa.