1 Corinthians 7:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati wina akuganiza kuti akumlakwira namwali wake amene adamtomera, ndipo ngati namwaliyo unamwali wake ukupitirira, tsono munthuyo nkuganiza kuti ayenera kumkwatira, angathe kuchita zimenezo, si kuchimwa ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wamkazi chosamuyenera, ngati palikupitirira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wina akuganiza kuti akumulakwira namwali yemwe anapalana naye ubwenzi, ndipo ngati chilakolako chake chikunka chikulirakulirabe, ndipo akuona kuti nʼkofunika kumukwatira, ayenera kuchita monga wafunira, kutero si kuchimwa ayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma wina akayesa kuti acitira mwana wace wamkazi cosamuyeoera, ngati palikupitirira pa unamwali wace, ndipo kukafunika kutero, acite cimene afuna, sacimwa; akwatitsidwe.