1 Corinthians 7:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe ngati wina, mwaufulu wake, popanda womukakamiza, watsimikiza kwenikweni kuti samkwatira namwali adamtomerayo, nayenso wachita bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wake wamkazi, adzachita bwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati wina motsimikiza mtima wake, popanda womukakamiza, koma akuchita mwa chifuniro chake, ndipo watsimikiza mtima kuti samukwatira namwaliyo, munthuyu akuchitanso chokhoza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwace, wopanda cikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa cifuniro ca iye yekha, natsimikiza ici mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wace wamkazi, adzacita bwino.