1 Corinthians 7:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati, nthaŵi yonse pamene mwamuna wake ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi mwamuna amene iye afuna, malinga ukwatiwo ukhale wachikhristu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati nthawi zonse pamene mwamuna wake ali ndi moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi wina aliyense amene akumufuna, koma mwamunayo akhale wa mwa Ambuye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mkazi amangika pokhala mwamuna wace ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.