1 Corinthians 8:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati iweyo amene uli wodziŵa udya m'nyumba yopembedzeramo fano, nanga tsono munthu wosadziŵa kwenikweni, atakuwona ukuchita zimenezi, kodi chimenechi sichidzamlimbitsa mtima kuti nayenso azidya chakudya choperekedwa kwa mafano?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti wina akaona iwe amene uli nacho chidziwitso, ulikukhala pachakudya m'Kachisi wa fano, kodi chikumbu mtima chake, popeza ali wofooka, sichidzalimbika kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ngati aliyense wachikumbumtima chofowoka akakuonani achidziwitsonu mukudya mʼnyumba yopembedzera mafano, kodi iyeyo sichidzamulimbitsa mtima kuti azidya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti wina akaona iwe amene uli naco cidziwitso, ulikukhala pacakudya m'kacisi wa fano, kodi cikumbu mtima cace, popeza ali wofoka, sieidzalimbika kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano?