1 Corinthians 8:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe si onse amene amadziŵa zimenezi. Ena adazoloŵera kupembedza mafano, ndipo mpaka lero akamadya chakudya choperekedwa kwa mafano, amaganiza ndithu kuti chakudyacho chidaperekedwadi kwa mafano. Tsono popeza kuti ali ndi mitima yofooka, mitima yaoyo imaipitsidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu chidziwitso sichili mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo chikumbu mtima chao, popeza nchofooka, chidetsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma saliyense amadziwa zimenezi. Alipo ena ozolowera mafano kwambiri mwakuti akadya chakudya chotere amaganiza kuti chakudyacho chinaperekedwa nsembe kwa mafano. Ndiye poti chikumbumtima chawo nʼchofowoka chimadetsedwadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu cidziwitso siciri mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo cikumbu mtima cao, popeza ncofoka, cidetsedwa.