1 Corinthians 9:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi sankanena zimenezi makamaka chifukwa cha ife? Adazilembadi chifukwa cha ife, pakuti wolima ndiponso wopuntha, onsewo amagwira ntchito yao ndi chiyembekezo chakuti nawonso adzalandirako kanthu pa zokolola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena achinena ichi konsekonse chifukwa cha ife? Pakuti, chifukwa cha ife kwalembedwa: popeza wolima ayenera kulima mwa chiyembekezo, ndi wopunthayo achita mwa chiyembekezo cha kugawana nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithu Iyeyo amanena za ifenso, kodi si choncho? Inde, izi anazilemba chifukwa cha ife, pakuti wolima ndiponso wopuntha, onsewo amagwira ntchito mwachiyembekezo chodzagawana zokololazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena acinena ici konse konse cifukwa ca ife? Pakuti, cifukwa ca ife kwalembedwa: popeza wolima ayenera kulima mwa ciyembekezo, ndi wopunthayo acita mwa ciyembekezo ca kugawana nao.