1 Corinthians 9:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati ena adziyesa kuti ndi oyenera kulandira zimenezi kwa inu, nanga ife sindiye oyenera koposa iwowo kuzilandira? Komabe kuyenera kumeneku sitidakugwiritse ntchito ai. Makamaka tidapirira zonse, kuwopa kuti tingachedwetse anthu mwa njira iliyonse kulandira Uthenga Wabwino wonena za Khristu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachita nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati ena ali ndi ufulu wothandizidwa ndi inu, kodi ife sitikuyenera kukhala nawo ufulu ochulukirapo? Koma ife sitinagwiritse ntchito ufulu umenewu. Mʼmalo mwake timangodzichitira chilichonse posafuna kutsekereza ena kumva Uthenga Wabwino wa Khristu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinacita nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingacite cocedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Kristu,