1 Corinthians 9:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ineyo sindinkagwiritsa ntchito konse lamulo limeneli. Ndiponso sindikulemba kalatayi chifukwa chofuna kuligwiritsa ntchito kumene. Kwenikweni ndikadakonda kuti ndife, kupambana kuti wina andichotsere chifukwa chimene ndimanyadira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine sindinachita nako kanthu ka izi; ndipo sindilemba izi kuti chikakhale chotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwachabe kudzitamanda kwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ine sindinagwiritse ntchito ufulu woterewu. Sindikulemba izi ndi chiyembekezo choti mundichitire zoterezi. Kuli bwino ndife kusiyana nʼkuti wina alande zomwe ndimazinyadira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine sindinacita nako kanthu kaizi; ndipo sindilemba izi kuti cikakhale cotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwacabe kudzitamanda kwanga.