1 Corinthians 9:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo tsono mphotho yanga ndi yotani? Mphotho yanga ndi yakuti ndikamalalika Uthenga Wabwino, ndizingoulalika mwaulere, osafuna kulandirapo malipiro aja amene ndikadayenera kulandira polalika Uthenga Wabwinowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mphotho yanga nchiyani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mphotho yanga ndi chiyani? Ndi iyi: kuti polalikira Uthenga Wabwino ndiwupereke kwaulere komanso kuti ndisagwiritse ntchito ufulu wanga polalikira uthengawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mphotho yanga nciani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.