1 Corinthians 9:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhaletu ena sandiyesa mtumwi, koma kwa inu ndine mtumwi ndithu, pakuti moyo wanu wachikhristu ndi umboni wakuti ndinedi mtumwi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati sindili mtumwi kwa ena, komatu ndili kwa inu; pakuti chizindikiro cha utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale kwa ena sindingakhale mtumwi, mosakayika ndine mtumwi kwa inu! Poti inu ndi chizindikiro cha utumwi wanga mwa Ambuye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati sindiri mtumwi kwa ena, komatu ndiri kwa inu; pakuti cizindikilo ca utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye.