1 Corinthians 9:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwa Ayuda ndidakhala ngati Myuda, kuti ndiŵakope. Ngakhale ineyo sindilamulidwa ndi Malamulo a Mose, komabe kwa Ayuda amene ali olamulidwa ndi Malamulowo, ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ndiŵakope.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa Ayuda ndimakhala ngati Myuda kuti ndikope Ayuda. Kwa olamulidwa ndi Malamulo ndimakhala ngati wolamulidwa nawo (ngakhale kuti sindine wolamulidwa ndi Malamulowo) kuti ndikope amene amalamulidwa ndi Malamulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;