1 Corinthians 9:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwa amene alibe Malamulo a Mose, ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ndiŵakope. Sindiye kuti ndilibe Malamulo a Mulungu ai, popeza kuti ndili nawo malamulo a Khristu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Khristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa amene alibe Malamulo ndimakhala wopanda Malamulo (ngakhale kuti sindine wopanda Malamulo a Mulungu koma ndili pansi pa ulamuliro wa Khristu) kuti ndikope wopanda Malamulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo twa Kristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.