1 Corinthians 9:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwa amene ali ndi chikhulupiriro chofooka, ndidakhala ngati wa chikhulupiriro chofooka, kuti ndiŵakope ofookawo. Kwa anthu onse ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ngati nkotheka ndikope ena mwa iwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa ofowoka ndimakhala wofowoka, kuti ndikope ofowoka. Ndimachita zinthu zilizonse kwa anthu onse kuti mwanjira ina iliyonse ndipulumutse ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwa ofoka ndinakhala ngati wofoka, kuti ndipindule ofoka, Ndakhala zonse kwa anthu onse, 1 kuti pali ponse ndikapulumutse ena.