1 Corinthians 9:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense wothamanga pa mpikisano wa liŵiro amadziletsa pa zonse. Iwowo amachita zimenezi kuti akalandire mphotho ya nkhata yamaluŵa yotha kufota. Koma mphotho imene ife tidzalandira, ndi yosafota.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense wochita mpikisano amakonzekera mwamphamvu. Amachita izi kuti alandire mphotho yankhata yamaluwa yomwe imafota. Koma ife timachita izi kuti tilandire mphotho yosafota.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma yense wakuyesetsana adzikaniza zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakubvunda; 3 koma ife wosabvunda.