1 Corinthians 9:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndimazunza thupi langa ndi kulisandutsa kapolo kuti nditatha kulalikira ena, ineyo ndingadzapezeke wosayenera kulandira nawo mphotho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma 4 ndipumpuatha thupi langa, ndipo ndiliyesa capolo; kuti, kapena ngakhale rdalalikira kwa ena, 5 ndingakhale votayika ndekha.