1 Corinthians 9:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi alipo msilikali womadzipezera yekha zofunika zonse? Kodi alipo munthu wobzala mpesa, koma osadyako zipatso zake? Kodi alipo munthu wokhala ndi ziŵeto, koma osamwako mkaka wake?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Msilikali ndani achita nkhondo, nthawi iliyonse, nadzifunira zake yekha? Aoka mipesa ndani, osadya chipatso chake? Kapena aweta gulu ndani, osadya mkaka wake wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndani angagwire ntchito ya usilikali namadzipezera yekha zofunika zonse? Kodi ndani amadzala mpesa koma wosadyako zipatso zake? Ndani amaweta nkhosa koma wosamwako mkaka wake?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Msilikari ndani acita nkhondo, nthawi iriyonse, nadzifunira zace yekha? Aoka mipesa ndani, osadya cipatso cace? Kapena aweta gulu ndani, osadyamkaka wace wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?