1 John 1:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse.