1 John 2:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu atate, ndikukulemberani, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Inu achinyamata, ndikukulemberani, chifukwa mwampambana Woipa uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamlaka woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu abambo, ndikukulemberani popeza kuti munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi. Inu anyamata, ndikukulemberani popeza kuti munagonjetsa woyipayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira iye amene ali kuyambir paciyambi. Ndikulemberani anyamata, popeza mwamlaka woipavo, Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.