1 John 2:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndimakulemberani inu ana, chifukwa Atate mumaŵadziŵa. Ndimakulemberani inu atate, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Ndimakulemberani inu achinyamata, chifukwa ndinu amphamvu, mau a Mulungu amakhala mwa inu, ndipo mwampambana Woipa uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamlaka woipayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana okondedwa, ndikukulemberani chifukwa mumawadziwa Atate. Abambo, ndikukulemberani chifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi. Inu anyamata, ndikukulemberani chifukwa ndinu amphamvu. Mawu a Mulungu amakhala mwa inu ndipo mumamugonjetsa woyipayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira iye amene ali kuyambira paciyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muti amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamlaka woipayo.