1 John 2:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti zonse za mʼdziko lapansi, zilakolako za thupi, zinthu zimene maso amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ciri conse ca m'dziko lapansi, cilakolakoca thupi ndi cilakolako ca maso, matamandidwe a moyo, sizicokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.