1 John 2:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ananu, ino ndi nthaŵi yotsiriza. Mudamva kuti kukubwera Woukira Khristu, ndipo tsopano aoneka kale ambiri oukira Khristu. Zimenezi zikutizindikiritsa kuti ino ndi nthaŵi yotsirizadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Khristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana anga, ino ndi nthawi yotsiriza, ndipo monga munamva kale kuti anthu okana Khristu akubwera, ngakhale tsopano okana Khristu ambiri afika kale. Zimenezi zikutisonyeza kuti ino ndi nthawi yotsiriza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana inu, ndi nthawi yorsirtza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana. Krisru akudza, ngakhale tsopano alipo okana Kristu ambiri; mwa ici tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi.