1 John 2:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adachita kuchoka pakati pathu, komabe sanali a gulu lathu kwenikweni. Pakuti akadakhala a gulu lathu, bwenzi akali nafebe. Koma adatichokera, kuti aonekere poyera kuti panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene anali wa gulu lathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amenewa anachoka pakati pathu, komatu sanali a mʼgulu lathu. Pakuti akanakhala a mʼgulu lathu, akanakhalabe nafe, koma kuchoka kwawo kunatisonyeza kuti sanali a mʼgulu lathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anaturuka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero 1 kuti aonekere kutr sali onse a ife.