1 John 2:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndakulemberani, osati chifukwa chakuti simudziŵa choona, koma chifukwa chakuti mumachidziŵa, ndipo mukudziŵanso kuti bodza silichokera ku choona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sindinakulemberani chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sindikukulemberani chifukwa choti simudziwa choonadi ayi, koma chifukwa choti mumadziwa choonadicho, ndipo mukudziwanso kuti bodza silichokera pa choonadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sindinakulemberam cifukwa simudziwa coonadi, koma cifukwa muddziwa, ndi cifukwa kulibe bodza locokera kwa coonadi.